Wokondedwa Moyo’we: Kodi ukudziwa kuti wapezeka wochimwa ndi Mulungu Woyerayo, ndi kuti kwaikidwa kwa iwe kufa? Ngati munthu wochimwa afuna kuithawa imfa ya muyayayi ndi kupulumutsidwa ku nthawi zosatha, iye ayenera kulandira chifundo cha Mulungu’chi. Chifundo chimatiteteza ife pa chirmene tikadalandira. Komatu Mulungu samangoika chifundo chake pa anthu popanda choyenereza ayi, ngakhale kuti chipulumutso nchaulere, chopanda mtengo wake (chosagula) ndiponso chosati nkuchigwirira ntchito. Chotiyenereza chakuti Mulungu atipatse ife chifundo chake chipezeka mu liu limodzi lokha: Lapani.
August 3, 2023 in Kusambira 5 minutes
Aliyense ayenera kudzifunsa funso lofunikali, “Kodi ndichite chiyani kuti ndipulumutsidwe?” Anthu ambiri ama-khulupirira kuti anapulumutsidwa kale, koma Yesu anati, “Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba: koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba” (Mateyu 7:21). Kuti tipulumuke tiyenera kukhulupirira kuti Yesu adzakhululukira machimo athu. Kenaka tiyenera kulapa machimowo, kukhala ndi moyo wopanda tchimo, ndiponso kukondana wina ndi mzake. Chifukwa cha kuchuluka kwa ziphunzitso zimene zimaphunzitsidwa ndi zipembedzo zosiyana-siyana, funso ili litha kufunsidwa, “Kodi choonadi ndi chiyani?” Kodi “Kubadwa Mwatsopano” Kumatanthauza Chiyani? Ndani Akusowa Kubadwanso Mwatsopano? Kulapa Chikhulupiriro ndi Kumvera
March 31, 2023 in Kusambira 4 minutes
Kodi nchiyani ichi chirikulasa m’moyo mwangamu? Kufunafuna mtendere ndi mpumulo kosalekezaku? Kusungulumwa ndimakumvaku? Ngakhale kuti ndiri mkati mwagulu Kulira kowawa uku ndi kwakuya ndi kwakukulu; Kuliraku ndi kwenikweni! Kwenikweni ndithu! Dziko lachabe kodi ungatonthoze kuliraku? Kodi chuma chimene wadziunjikiracho chakupezera iwe mtenderewu? Ndipo iwenso tatero ndi kulira! Taona! chuma, kusangalala, ndi kunyada, Zimene zitchulidwa zangokhala mwadzina chabe! Izi zilephera kukhutitsa! Moyo wanga wokondedwawe! Uku kukhalenso kulira kwako! Kodi ukuona kuti irnfa ya muyaya ili pafupi, Ngati Mulungu sakupatsa mtendere? Iwe ukhale pa mbali ya oikidwa m’manda pamodzi ndi lye; Ndipo funitsitsa kumasulidwa ku uchimo, Ndi kukakhala ndi Iye potsiriza pake!
March 31, 2023 in Kusambira 4 minutes
Zimene zalembedwa m’munsi ndi zizindikiro zowonetsa moyo wa kudzikonda. Mzimu Woyera yekha ndi amene angathe kukutanthauzirani izi aliyense payekhapayekha. Pamene mukuwerenga, dziyezeni nokha pa maso penipeni pa Mulungu. KODI MUMAWONA IZI M’MOYO MWANU: ●Mzimu wobisika wa kunyada kapena wodzikuza powona mwapambana kapena mwapatsidwa udindo; chifukwa chakuti munaphunzira bwino kapenanso mawonekedwe anu; chifukwa cha nzeru kapena mphatso zanu; mzimu umene umadziwona ngati wofunika ndipo wosadalira ena? Miyambo 16:18; 20:6; 25:14; Aroma 12:3; Yakobo 4:6. ●Zachipamaso, kusowa moyo wa uzimu; kusakhudzika ndi miyoyo yotayika; kusowa mphamvu ya Mulungu? Mateyu 15:14; Timoteo 3:5; Chivumbulutso 2:4; 3:1. Kuti ndipulumutsidwe ku kudzikonda kwanga; Ambuye!
March 31, 2023 in Kusambira 3 minutes