Nthawi ino muli ndi moyo;mukupuma;mukudya ndi kumwa madzi tsiku ndi tsiku; mukutha kuyendayendakugwira ntchito zanu ndi kumagona. Mwina mukukhala moyo wokandwa mwina wodandaula chifukwa cha mabvuto. Tsiku ndi tsiku dzuŵa likutuluka ndipo likuloŵa; ku malo ena mwana akubadwa, komanso kumalo ena wina akumwalira.
PAMENEPA TIONA KUTI ZONSE ZA MOYO
WAPANSI PANO NDI ZOSAKHALITSA.
KOMA,
NDIKADZAFA NDIDZAPITA KUTI?
Kaya ndine Mkhristu wofooka
kapena wopembedza ku Chisilamu
kapena wopembedza ku Chibuda
kapena wopembedza ku Chiyuda
kapena wopembedza mizimu ya makolo
kapena wopembedza chimodzi cha zipembezo
zambiri zimene tingazitchule,
kapena wosapembedza kumene –
Koma tiyenera kuyankha funso lofunika kwambirili, chifukwa pakutha pa moyo wapansi pano, wa kanthawiwu, munthu ayenera kupita kwawo kumene kuli kokhalitsa.
NANGA KUMENEKU NDI KUTI?
Popeza kuti: Manda amene mudzakwiriridwamo sadzakwirira mzimu wanu, ngakhale mutadyedwa ndi chilombo kepena mbalame, sizidzameza mzimu wanu, kaya mudzamizidwa ndikufera mnyanja, mzimu wanu siudzamira mmadzimo, ngakhale thupi lanu litatenthedwa ndi moto, mzimu wanu siungapsye.
MZIMU WANU SIUDZAFA!
MULUMGU AMENE ANALENGA
KUMWAMBA NDI DZIKO LAPANSI
AKUTI, “MIZIMU YONSE NDI YANGA.”
Ku malo ena utatha moyo uno, “INUYO” mudzakomana ndi zones zimene munachita mdziko lapansi mmoyo wanu wathupi – zabwino kapena zoipa.
Tikhoza kumapembedza mokhulupirika.
Tikhoza kumva chisoni ndi zolakwa zathu.
Tikhoza kubwezera zimene tinaba.
Zoonadi zonsezi ndi zoyenera –
KOMA –
Sitingathe kudziyanjanitasa ndi Mulungu chifukwa cha zochimwa zathu. MULUNGU wakumwamba, woŵeruza mwa chilungamo padziko lonse lapansi amadziŵa machismo anu ndi moyo wanu – palibe chobisika kwa Iye. Inu, ndi machismo anu simungathe kukaloŵa mu UFUMU ndi ULEMERERO wa dziko lirinkudza.
KOMA –
Mulungu wakumwambayu ndi Mulungu wachikondi. Iye wakonza njira yopulumutsira moyo ndi Mzimu wanu. Simudzaponyedwa ku chionongeko, kumoto, ngati mupemphera ndi kulapa machismo anu kwa Mulungu. Mulungu adzakukhululukirani kupyolera mwa Mwana wake Yesu Khristu. Yesu anazunzidwatu chifukwa cha zochimwa zanu, ngati mulambira ndi kupemphera kwa Iye yekha, adzalankhula za mtendere mmoyo wanu ndi kukupatsani moyo wa ulemerero mutafa pansi pano. Koma Yesuyo – amene ali Mwana wa Mulungu wamoyo, ayenera kukhala Mpulumutsi wanu choyamba. Mukatero ndiye kuti muli nacho chitsimikizo choti mudzakhala kudziko losatha, la chimwemwe chachikulu ndi mpumulo wa mzimu wanu. Koma HO!, dzenje la chionongeko ndi moto wosatha ziyembekezera iwo amene mmoyo uno akukana chikondi cha chipulumutso cha Ambuye Yesu. Sipadzakhalanso mwaŵi wolapa kapena kupulumuka mutafa. “Pamenepo idzauzanso a kudzanja lake lamanzere aja kuti, Chokani, inu anthu otembereredwa, Pitani kumoto wosatha umene Mulungu anaukonzera Satana ndi angelo ake” (Mateyu 25:41). “Ndipo wanychito wopanda pakeyu, mponyeni kunja kumdima, Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano” (Marko 25:30). Mulungu, m’Buku Lopatulika, akuchenjezeratu mokwanira za chiŵeruzo chadziko lapansi chimene chiri pafupi. Mau a Mulungùŵa akuneneratu kuti lisanafike tsiku loyembekezeka la chiŵeruzolo padzakhala zizindikiro zoonekeratu zomwe zinanenedwa kale. Asanadze iye kudzakhala nkhondo ndi mbiri za nkhondo, kuukirana kwa mitundu, wina ndi unzake – sipadzakhalanso njira zakuthetsera kusiyana maganizo ndi kusamvana kwawo. Kudzakhala zibvomezi mmalo osiyanasiyana ndi milili ya matenda woopsya. Zonsezitu zakwanitsidwa kale mzaka zino. Mau a Mulungu aneneranso kuti anthu ochimwa adzachita zoipitsitsa ndipo sadzamvera chenjezo lirilonse, ndipo adzakonda chitayiko koposa Mulungu. Tikumbukire kuti Mfumu yathu yaikulu ndi ya chiŵeruzo cholungama siidzaganizira za kulemera kapena kusauka kwa munthu, kutchuka kwake kapena ulemu umene ali nawo, khungu kapena mtundu, kapena chipembedzo. Tsiku lina tidzaima osoŵa cholankhula pamaso pa Mlengi ndi Mfumu yathu, ngati tinyozera kubvomereza chipulumutso chimene watipatsa. Nthawi ya ulemerero wosatha imene ikubwerayo sikudzakhala kuŵerenga nthawi, masiku, nyengo kapena zaka. Utsi wa msautso wa anthu ochimwa ndi wokana Mulungu udzafuka nthawi zones osaleka – mmene nthawi yomweyo chimwemwe, mtendere, mpumulo ndi kuyimba kwa opulumutsidwa zidzakhalanso zosatha nthawi zones kumwambako. Dzisankhireni nokha nthawi ino! Ngati mukuganiza za nthawi ina, ndiye kuti mukuchedwa. Ŵerengani Uthenga Wabwino wa Mateyu, Marko, Luka ndi Yohane, mukatero ŵerengani Chipangano Chatsopano chonse. Kenako Buku Lopatulika lonse.