Nkhani imodzi ya kutsitsimuka kwa akufa, imene inandichititsa chidwi kwambiri ndi nkhani ya George Lenokisi. Iye anali wakuba wodziwika amene anakhala ku boma la Jefferson County, ankakonda kuba abulu. Iye anali mundende atamangidwa kachiwiri. Poyamba anamangidwa ndi boma la Sedgwick County chifukwa cha mlandu womwewo, kuba abulu.
Pakati pa chaka cha 1887 ndi 1888 inali nyengo yozizira, iye adali kugwira ntchito mumgodi wa malasha. Pa malo pamene iye adali kugwira ntchito padali poopsa kwa iye. Kotero adachita lipoti kwa mkulu wa ntchito, iye ataona malowo adam'uza kuti malowo ali bwino, ndipo ayenera kupitiriza kugwira ntchito yake. Iyeyu adamvera, koma sadapitirira kugwira ntchito nthawi yaitali, pamenepo denga la mgodi lidagwa lidamukwirira. Adakhala pomwepo kwa maola awiri.
Pa nthawi ya chakudya cha madzulo adasowa. Atamufufuza anam'peza pansi pa zinyalala za denga la mgodi. Atamuchotsa dokotala wa m'ndendemo adam'yeza, nam'peza kuti munthuyo wafa kale. Thupi lake adalitengera kuchipatala komwe adalisambitsa bwino ndi kuliveka zovala, pokonzekera kukaliika ku manda. Adamukonzera bokosi loyembekezera kugonamo iye ndipo adafika nalo kuchipatala. Abusa a kundende adafika kudzachita mwambo wa maliro. Woyang'anira za m'ndende adauza akaidi ena kuti ayenera kunyamula mtembo uja ndi kuwuika m'bokosi. Iwowa adamvera, nanyamula mtembowo, ena ku miyendo ena kumutu, koma ali pafupi kuti afike pamene padali bokosi amene adanyamula kumutu adapunthwa mwangozi nagwetsa mtembowo. Mutu wa mtembowo udagunda pansi ndipo onse amene adali pamalopo adadabwa kwambiri pakumva wakufa uja akubuula. Nthawi yomweyo maso ake adatseguka naonetsa kuti ali ndi moyo. Dokotala adaitanidwa kuti abwere. Zitatha mphindi makumi atatu (30 minutes) dokotala adafika, napeza kuti wakufayo adaitanitsa madzi akumwa ndipo adali pakati pa kumwa madziwo.
Nthawi yomweyo bokosi lija lidachotsedwa ndipo lidagwiritsidwa ntchito poikamo mtembo wa mkaidi wina. Kenaka adamuchotsa zovala zake za kumanda zija ndipo adamupatsa zovala zake za kundende. Atamuyeza adapeza kuti mwendo wake umodzi udathyoka malo awiri, ndiponso anali ndi mabala. Adakhala kuchipatala miyezi isanu ndi umodzi. Atachira adatumizidwanso kukapitiriza ntchito yake ku ndende.
Wandende mnzake wa Lenokisi adandiuza chinthu cha chilendo chomwe chidam'chitikira pa nthawi yomwe adali ngati wakufa. Nkhaniyi idandichititsa chidwi moti ndidafunitsitsa kukomana naye Lenokisi kuti ndimve nkhaniyi kuchokera pakamwa pake. Mwayi woti ndikomane naye sudapatsidwe kwa ine kwa miyezi ingapo, koma kenaka ndidakomana naye. Nditachotsedwa pantchito ya mu'mgodi ndidapatsidwa ntchito yolemba malipoti ena kuofesi ina yakundende. Tsiku lina nkhani yakuuka kwa akufa kwa munthu uja idakambidwa, nthawi yomweyo adadutsa pakhomo paofesi, ndipo adandilozera kwa iye. Posakhalitsa ndidam'patsa kalata yoti afike kumene ndidali kugwira ntchito. Atafika, ndidali ndi nthawi yokambirana naye, ndipo kuchokera pakamwa pake ndidamva nkhani yake yodabwitsa. Adali wachinyamata wosapyolera zaka makumi atatu, koma anakhwima m'makhalidwe a umbava. Adali munthu wophunzira bwino komanso wanzeru.
Mbali yodabwitsa ya nkhani yake idachitika panthawi imene adali wakufa. Popeza ndidali wotola nkhani mwachidule, ndidali kulemba zonse zomwe adali kundiuza.
Iye adati: “ Kuyambira m'mawa wonse ndidali nditadziwa kuti kanthu kena koopsya kadzachitika. Chifukwa cha nkhawa imeneyi ndidapita kwa woyang'anira wamkulu wa mumgodi, Bambo Grason, kuti ndimulongosolere momwe ndidali kumvera. Ndidam'pempha kuti adzaone malo omwe ndidali kugwirapo ntchito yokumba malasha. Adabwera, nakhala ngati wapimadi malowo, nandilamula kuti ndiyenera kupitiriza kugwira ntchito. Adandiuza kuti palibe choopsa chili chonse, naganiza kuti mutu wanga wasokonekera. Ine ndidabwerera ku ntchito yanga, ndipo ndidali kukumba kwa ntahwi yochepa, pamenepo ndidaona mwadzidzi kunali mdima waukulu. Kenaka padaoneka ngati chitseko chachitsulo chachikulu chidatseguka, ndipo ndidalowa pa khomo lake. Pamenepo ndidadziwa m'moyo mwanga kuti ndidali wakufa ndipo ndidali m'dziko lachilendo. Sindidathe kuona munthu wina ali yense kapena kumva china chilichonse, ayi. Mphamvu ina yosadziwika kwa ine idandiyendetsa kuchoka pakhomopo ndipo ndidayenda patali kufika m'mphepete mwa mtsinje waukulu. Kudali ngati usiku pamene pali nyenyezi zambiri, sikudali kowala kweni-kweni kapena mdima. Sipadapite nthawi yaitali, ndili kutsidya la mtsinjewo, ndidamva phokoso lotakasidwa madzi popalasa bwato. Posachedwa munthu amene adali m'bwatomo adapalasira kufika pafupi ndi pomwe ndidaima.
“Nthawi imeneyo ndidali wopanda mawu. Iye adandiyang'ana kamphindi kochepa, nati kwa ine, 'ndabwera kudzakutenga,' nandiuza kuti tikwere bwatolo kuti tiolokere tsidya lina. Ndidamumvera. Padalibe mawu ena amene adalankhulidwa. Ndidali kufuna kuti ndimufunse dzina lake ndiponso kumene ndili, koma sindidathe chifukwa lilime langa lidamamatira m'kamwa mwanga, kotero kuti sindidathe kunena liwu lililonse. Kenaka tidafika tsidya lina la mtsinjewo ndipo ndidachoka m'bwatomo. Nditaturukamo wopalasa bwato uja anandikanganukira kumaso kwanga, nandichokera.
“Atandisiya choncho, ndidasowa chochita. Poyang’ana patsogolo panga, ndidaona njira ziwiri zidaloza ku chigwa cha mdima. Njira imodzi idali yotambalala imene imaoneka kuti ndi yotakata. Njira ina idali yopapatiza yopita mbali ina, koma ine ndidatsata njira yaikulu yotakata ija. Sindidapite patali pamene ndidaona kuchuluka kwa mdima udali nkukulabe. Komabe ndidali kuona kuwala kochokera patali, potero ndidaunikiridwa pa ulendo wangawo.
“Posachedwa ndidakomana ndi chinthu china, maonekedwe ake sindingathe kulongosola, koma ndingalongosole pang’ono maonekedwe ake oopsya. Maonekedwe ake adali ngati munthu, koma adali wamkulu koposa munthu aliyense amene ndidamuonapo. Utali wake udali monga ngati mamita atatu. Adali ndi mapiko akulu kumbuyo kwake. Adali wakuda monga ngati malasha omwe ndinali kukumba. Adali wamaliseche wosavala chirichonse. M’dzanja lake adagwira nthungo yotalika pafupifupi mamita asanu. Maso ake adawala ngati mipira ya moto. Mano ake adali oyera kwambiri ndipo utali wake monga ngati inchi imodzi. Mphuno yake idali yaikulu ndithu yotambalala yokhala yophwaphwatika. Tsitsi lake lidali lokhakhala, losaoneka bwino, lalitali, ndipo linagwera m’mapewa ake akulu. Mawu ake anabangula monga mau a mkango.
“Idali nthawi yowala mu mdimamo imene ndidamuona poyamba. Ine ndidanjenjemera kwambiri monga tsamba la mtengo logwedezeka ndi mphepo. Adakweza nthungo m’dzanja lake kuloza kwa ine nakhala ngati afuna kundiponyera. Mwadzidzidzi ndidaima. Ndili wonjenjemera chomwecho, adanena ndi mawu woopsya amene ndikuwakumbukirabe, nandiuza kuti ndimutsate iye chifukwa watumidwa kuti anditsogolere pa ulendo wangawo. Ndipo ndidamutsata. Ndi chiyani chomwe ndikadachita? Titayenda patali pang’ono, phiri lalikulu lidaonekera patsogolo pathu. Lidaoneka phiri longa logawidwa pakati, ndipo pa mbali ina ya phirilo inali khoma lalitali. Pakhomapo padali mau olembedwa: ’MALO A GEHENA’. Wonditsogolera adafika pakhoma la phirilo nagogoda katatu ndi chogwirira cha nthungo yake. Ndipo chitseko chachikulu chidatseguka cham’tsogolo, ndipo tidalowa mkati. Pamenepo adanditsogolera kupyolera mkati mwa phirilo.
“Pa kanthawi tidayenda mumdima waukulu. Ndidali kumva mgugu wa mapazi oyenda kotero kuti ndidatha kutsatira wonditsogolerayo. M’njira yonseyo ndinali kumva kubuula monga ngati wina alinkufa. Popitirira ndi ulendo wathu kuliraku kudali kuchuluka, ndipo onsewo adali kulira poitanitsa, ‘Madzi, madzi, madzi.’ Tsopano titafika pakhomo lina, popitirira, ndidamva mau wolira mochuluka ngati anthu okwana zikwi chikwi patali. Ndipo kulirako kudalinso kupempha, ‘Madzi, madzi, madzi.’ Posachedwa khomo lina lalikulu lidatseguka wonditsogolera atagogoda. Ndidapeza kuti tidayenda mopyola mkati mwa phiri lija, ndipo ndidaona chigwa chachikulu chili patsogolo panga.
“Pamalo amenewa wonditsogolerayo adandisiya ndekha, napita kukatsogoleranso mizimu ya anthu ena otayika kunjira yomwe tidadzerayo. Ndidakhala pa chigwa chotsegukacho kanthawi pamene munthu wina wokhala ngati woyamba uja adabwera kwa ine; koma m’malo mokhala ndi nthungo, iye adabwera ndi lupanga lalikulu. Iye adabwera kudzandiuza za chionongeko changa cham’tsogolo. Adalankhula ndi mau oopsya amene adakhudza moyo wanga. Adati, ‘Iwe, uli ku Gehena. Chiyembekezo chako chonse chathawa. Pobwera kuno udayenda kupyola m’phirimo, ndipo udali kumva kulira kwa anthu otayikawo, amene adali kupempha madzi kuti athe kuziziritsa malilime awo otenthedwa. Panjira imeneyo pali khomo lolowera kupita ku nyanja ya moto. Posachedwa kumeneko kudzakhala chionongeko chako. Musanaperekezedwe ku malo amazunzo awo, kumene simudzatulukanso (chifukwa kulibenso chiyembekezo kwa amene alowamo) mudzaloledwa kuima malo achigwa ngati ano, kumene kwapatsidwa kwa onse otaika, kuonetsedwa zabwino zomwe akanazilandira, koma m’malo mwake alinkulandira chilango.
“Zitatha izi ndidapezeka ndiri ndekha. Kapena chifukwa cha kuopsedwa kwambiri pa njira, sindikudziwa, koma tsopano ndidapezeka wolefuka. Kufooka ndi kusamva kudagwira thupi langa, mphamvu zanga zidachoka, ziwalo zanga zidalephera kulimbitsa thupi langa. Ndidathedwa, ndipo ndidagwa pansi. Ndidakhala ngati ndakomoka, monga munthu wogona koma ali ndi moyo, ndipo ndidaona ngati ndikulota. Poyang’ana kumwamba patali ndi ine, ndidapenya mzinda wokongola ndithu womwe timauwerenga m’Buku Lopatulika. Makoma ake adanyezimira ngati miyala ya yaspi ndipo pambali pa mzindawo ndidaona malo akulu okutidwa ndi maluwa okongola kwambiri. Ndidaonanso mtsinje wa moyo ndi nyanja yowala ngati galasi. Ndipo angelo ochuluka adali kulowa ndi kutuluka pa zipata za mzindawo, ali kuimba nyimbo zokoma. Pakati pawo ndidaona mayi wanga wokondedwa amene adafa zaka zapitazo ndi mtima wawo wosweka chifukwa cha zoipa zomwe ndidali kuchita. Mayi adandiyang’ana nandikodola kuti ndipite komwe kudali iwo. Koma ine sindidathe kusuntha pomwe ndidali. Kudaoneka ngati ndili ndi chinthu cholemera kwambiri chomwe chidandikanikiza pansi. Pamenepo mphepo yabwino idawomba kuloza kwa ine ndi kununkhira kochokera m’maluwa okongola aja kudandifikira ine. Ndidamva kuyimba kokoma kwa angelo, ndipo ine ndidalira ndi kunena, ‘Ndikadakhala m’modzi wa iwo.’
“Ndidakali kumwera chikho chokomachi poona zokoma zonse, mwadzidzidzi chidachotsedwa kukamwa kwanga. Munthu uja anandidzutsa kutulo tanga, ndipo nandichotsa ku dziko labwino lomwe ndidali kuona masomphenya. Anandiuza kuti, ‘Ndi nthawi tsopano yokalowa komwe iwe udzakhala. Munditsate ine.’ Pamene ndidayamba kuyenda, ndidalowanso munjira ya mdima. Ndidamtsatira wonditsogolera kanthawi, pamene tinafika pakhomo lotseguka pambali. Popitirira pamenepo tidapezeka tili kulowa pakhomo pena, ndipo taonani ndidaona nyanja ya moto! Nditapenya polekezera maso anga ndidaonadi nyanja ya moto ndi miyala ya moto. Mafunde akulu a moto adali kukweranakwerana, funde lina pa linzake. Malawi a moto adali kukwera m’mwamba monga mafunde a m’nyanja owinduka ndi mphepo yaikulu. Ndidapenya anthu alikulimbana ndi mafunde a motowo, koma mafundewo adali kuwakanikiza pansi pakuya munyanja ya moto. Pamwamba pa mafunde akulu a moto padaoneka anthu, kwa kanthawi adali kutukwana moipitsitsa Mulungu wolungamayo. Kulira kwao kolilira madzi kudali komvetsa chisoni. M’nyanja yamoto imeneyi mudali kumveka mau olira ndi kulira kosalekeza kuchokera ku mizimu yotaikayo.
“Pamenepo ndidatembenuza maso anga kuyang’ana pakhomo pamene ndidalowapo posachedwa, ndipo ndidawerenga mau olembedwa motere: ‘Malo ano ndi a chilango; kunthayi yosatha.’ Posakhalitsa ndidaona nthaka ilikuchoka ku mapazi anga, pomwepo ndidapezeka ndili kumira munyanja yamoto. Ludzu losaneneka lofuna madzi lidabwera kwa ine. Ndili kuitanitsa madzi, maso anga adatseguka, ndipo ndidapeza kuti ndili ku chipatala cha kundende.
“Sindidauze aliyense nkhani imeneyi kale lonse, chifukwa ndidali kuchita mantha kuti akulu oyang’anira m’ndende akadandiganizira kuti ndazungulira mutu, ndi kundisekera m’chipatala cha amisala. Ine ndidapyola mu zonsezi, ndipo ndili wokhutitsidwa kuti Kumwamba kulipo, Gehena ilipo, ndi Gehena yakaleyo imene Buku Lopatulika limanena nthawi zonse. Koma choonadi ndi ichi, ine sindidzapitanso ku malo a Gehenawo ayi.
“Pamene ndidatsegula maso anga mu chipatala ndi kuona kuti ndili ndi moyonso mdziko lino, nthawi yomweyo ndidapereka mtima wanga kwa Mulungu, ndipo ndidzakhalabe Mkhristu mpaka imfa. Sindidzaiwala konse kuopsa kwa Gehena ndi zokoma zakumwamba zomwe ndidaziona. Ine ndakonzeka kukakomana ndi wokondedwa mayi anga omwe ali kale komweko. Ndipo ndidzaloledwa kukhala pansi pa m’mbali mwa mtsinje wokongolawo, ndipo ndidzatha kuyenda ndi angelowo kuwoloka chigwacho ndi kupyola mapiri omwe akutidwa ndi kununkhira kwa maluwa omwe kukongola kwake kosayerekeza ndi kanthu kalikonse ka m’dziko lino lapansi. Ndidzakhala ndikumvera nyimbo za anthu owomboledwa. Panopa ndasiya zokondweretsa za dziko zomwe ndidayendamo kale ndisadabwere ku ndende, chifukwa zokoma za Kumwamba zidzaposa zonsezo. Ndawasiyanso abwenzi omwe ndidali kuchita nawo zoipa, ndiyenera kugwirizana ndi anthu a makhalidwe abwino ndikadzatuluka mundende.”
Tikupereka nkhani imeneyi kwa awerengi onse monga momwe ife tidailandira kwa Bambo Lenox. Tikuzindikira kulephera kwa maganizo amunthu kufotokoza za kumwamba kapena Gehena. Choncho nkhani ya Bambo Lennox singakhale kulongosola kwenikweni kwa Gehena koma m’malo mwake ndi chithunzithunzi cha umuyaya. Mulungu adalitse umboniwu pakudzutsa miyoyo yambiri yotayika.
Ha! Kodi anthu angakayike bwanji kuti kuli Gehena? Tili ndi Buku Lopatulika ndilo mau a Mulungu ndiponso mabvumbulutso monga a Bambo Lenokisi amene aphunzitsa za Gehena. Abambo ndi amai, khalani chete! Choonadi chilipo! Moyo wanu udzawerengedwa! Mulungu akufuna kukupulumutsani, ndipo adzaku-khululukirani ngati muvomereza kuti ndinu wochimwa. Njira yokhayo yoloza kuchipulumutso ndi kutsukidwa kuchokera ku machimo pakuvomereza mwazi wa Yesu Kristu monga nsembe ku machimo anu. Mukalandira chikhululukirochi kuchokera kwa Mulungu, Adzakupatsani mtendere ndi mpumulo m’mtima mwanu. Mungakhale womasuka m’moyo uno, komanso wokonzeka kulandira chisangalalo cha kumwamba m’malo mwa ku khala ku Gehena osati masiku awiri okha koma m’paka muyaya.
Fanizo la mwini Cuma ndi Lazaro waumphawi
Luka 16:19-31
“Ndipo panali munthu mwini chuma amavala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse; ndipo wopemphapempha wina, dzina lake Lazaro, adaikidwa pakhomo pake wodzala ndi zilonda, ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini chumayo; komatu agalunso anadza nanyambita zilonda zake. Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka kuchifuwa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, naikidwa m'manda.
“Ndipo m'dziko la akufa anakweza maso ake, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m'chifuwa mwake. Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti aviike nsonga ya chala chake m'madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m'lawi ili la moto. Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi. 26Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikulu, kotero kuti iwo akufuna kuoloka kuchokera kuno kunka kwa inu sangathe, kapena kuchokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife, sangathenso. Koma anati, Pamenepo ndikupemphani, Atate, kuti mumtume kunyumba ya atate wanga; pakuti ndili nao abale asanu; awachitire umboni iwo kuti iwonso angadze kumalo ano a mazunzo. Koma Abrahamu anati, Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo. Koma anati, Iai, Atate Abrahamu, komatu ngati wina akapita kwa iwo wochokera kwa kufa adzasandulika mtima. Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.
Malemba ena: Chivumbulutso 21:7-8, Chivumbulutso 20:10,12,13; 2 Petro 3:10-12.