Aliyense ayenera kudzifunsa funso lofunikali, “Kodi ndichite chiyani kuti ndipulumutsidwe?” Anthu ambiri ama-khulupirira kuti anapulumutsidwa kale, koma Yesu anati, “Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba: koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba” (Mateyu 7:21). Kuti tipulumuke tiyenera kukhulupirira kuti Yesu adzakhululukira machimo athu. Kenaka tiyenera kulapa machimowo, kukhala ndi moyo wopanda tchimo, ndiponso kukondana wina ndi mzake. Chifukwa cha kuchuluka kwa ziphunzitso zimene zimaphunzitsidwa ndi zipembedzo zosiyana-siyana, funso ili litha kufunsidwa, “Kodi choonadi ndi chiyani?”
Kodi “Kubadwa Mwatsopano” Kumatanthauza Chiyani?
Anthu ambiri amayesa kutumikira Ambuye asanabadwe mwatsopano, koma amenewo, apulumukadi? Yesu anati, “Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu” (Yohane 3:3). Pamene Yesu anachoka kudziko lapansili, anatuma Mzimu Woyera. “Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa dziko lapansi za machimo, ndi za chilungamo, ndi za chiweruziro” (Yohane 16:8). Mzimu Woyera adzathandiza munthu kuti azindikire uchimo wake. Munthuyo akazindikira machimo ake, amamva kulemedwa ngati wanyamula katundu wolemera, ndipo amamva kutsutsika mu mtima wake. Ngati adzichepetsa, ndipo pokhulupirira Yesu akalilira kwa Mulungu ndi mtima wake wonse, pamenepo Mulungu adzamu-khululukira. “Chifukwa chache lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu” (Machitidwe 3:19). Kulapa machimo ndi kumva chisoni chifukwa cha machimowo, kuwasiya, kutembenuka mtima ndi kuyamba moyo watsopano. Izi zikachitika, Mzimu Woyera umalowa mu mtima ndipo munthuyo wabadwa mwatsopano. “Chifukwa chache ngati munthu ali yense ali mwa Kristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano” (2 Akorinto 5:17).
Ndani Akusowa Kubadwanso Mwatsopano?
“Pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu” (Aroma 3:23) Modzazidwa ndi Mzimu Woyera, mneneri Yesaya analosera za chipsinjo cha Ambuye wathu Yesu chifukwa cha machimo a anthu onse. Anati, “Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m’njira ya mwini yekha” (Yesaya 53:6). Yesu ananena momveka bwino kwa Nikodemo amene anafuna choonadi kuti munthu angathe kuona ufumu wa Mulungu pokhapokha atabadwa mwatsopano. Kubadwa kumeneku mwa uzimu ndiye ntchito ya Mzimu Woyera. Onse amene afuna kupulumutsidwa ayenera kubadwa kotere.
Onse amene alikutopa ndi kulema ndi chipsinjo cha machimo awo akuitanidwa kubwera kwa Yesu kuti apeze chikululukiro. Yesu akuitana: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani gori langa, ndipo phunzirani kwa Ine; cifukwa ndiri wofatsa ndi wodzi-chepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti gori langa liri lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka” (Mateyu 11:28-30). Yesu anavutika, nakhetsa mwazi wake, ndipo anafa pa mtanda “chifukwa cha machimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi” (I Yohane 2:2).
Kulapa
Kuti tibwere kwa Ambuye Yesu ndi mtima, moyo, maganizo, ndi mphamvu yathu yonse; tiyenera kulapa, kuvomereza machimo athu, ndi kubwezera zomwe tinaba. “Wobisa machimo ache sadzaona mwai; Koma wakuwabvomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo” (Miyambo 28:13). “Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire macimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chiri chonse” (I Yohane 1:9). Ngati tinalakwira anzathu, tiyenera kuvomereza machimo athuwo ndipo kubwezera zomwe tinatenga za anthu ena ndi kofunika. “Ndipo Zakeyu anaimirira nati kwa Ambuye, Taonani, Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogawika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndimbwezera kanai” (Luka 19:8).
Chikhulupiriro ndi Kumvera
Ife titabadwa mwatsopano, timayesetsa kukhala okhulupirika m'moyo wathu wachikhristu. Yesu anaphunzitsa ophunzira ake motere, “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wache, nanditsate Ine” (Mateyu 16:24). Ife tachenjezedwanso kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi (Yakobo 1:27). “Musakonde dziko lapansi, kapena za m'dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichiri mwa iye. Pakuti chiri chonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi” (1 Yohane 2:15-16).
Mkhristu adzatha kukwanitsa zimenezi potsata chitsogozo cha Mzimu Woyera. Mzimu Woyera udzam'tsogolera ndi kum'patsa mphamvu kuti akhale ndi moyo wokondweretsa Mulungu. “Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m’choonadi chonse” (Yohane 16:13). Zotsatira za kumvera Mzimuyo ndiye mtima wosinthika; munthuyo adzakhala ndi chikhulupiriro chomvera Mulungu. “Ndipo moturuka mwa ntchito chikhulupiriro chidayesedwa changwiro” (Yakobo 2:22). Pamenepo mkhristuyo amadzipereka kwa Yesu m'malo mwa kudzisangalatsa yekha.
Mkhristuyo adzakhala ndi chikondi cheni-cheni chifukwa Mzimu Woyera amakhala m’kati mwa mtima wake. Adzafuna kuyanjana ndi Akhristu ena amene anabadwa mwatsopano. Chiyanjano chimenechi chimalimbikitsa iwo kugawana motsegula mtima. Zimenezi zimachirikiza mkhristuyo ndipo zimam’thandiza kuti akule m'moyo wake wachikhristu.
Tikabadwa mwatsopano mayina athu amalembedwa m'buku la moyo. “Ndipo ngati munthu sanapezedwa wolembedwa m'buku la moyo anaponyedwa m'nyanja yamoto” (Chivumbulutso 20:15). Machimo athu akakhululukidwa timamva chimwemwe ndi mtendere m’mitima yathu. Satana adzayesa kutibera mphatso ya chipulumutso chathu potiyesa kuti tikhale osamvera, koma Mulungu analonjeza kuti adzatiteteza ndi kutilanditsa ngati tikhala okhulupirika. “Chifukwa chache tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa” (Aroma 8:1). “ Chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza” (1 Timoteo 4:8).