Chiyero Chikondi Kukhulupirirana Makomo osangalala
Chilakolako Manyazi Mantha Makomo olekana Kusungulumwa
Chiyero cha maganizo, chikumbumtima ndi thupi ndi chinthu chopindulitsa m’moyo wa munthu. Ngakhale chiyero chokha sichitanthauza umulungu, koma ndi chipatso cha chikhristu ndi dalitso kwa mtundu wa anthu. Chifukwa cha kuperewera kwa chikhalidwe chabwino amayi ndi abambo lero akulola kukhudzidwa ndi chikhalidwe chimene Buku Lopatulika limanena kuti ndi tchimo. Chikhalidwe chavomerezedwa ngati njira yabwino m’moyo uno ndi anthu ambiri. Chimene Mulungu akunena kuti tchimo, sichikhalanso ngati tchimo. Nanga zotsatira zake zidzakhala zotani?
Wailesi ya kanema, zithunzi zoipa ndi zolembedwa zadzadzidwa ndi zovulazana, chigololo ndi machitidwe ambiri onyansa. Machitidwe oipawa afikanso m’makomo ngati zosangalatsa. Mitima ya amayi, abambo ndi ana yachulukira kukhala ndi maganizo a zilakolako ndi kukhumba zoipa. Chomvetsa chisoni chakuti makhalidwewa aku-pezekanso makomo ngakhale mwa iwo amene amati, “Ndife akhristu” masiku ano.
Mawu a Mulungu amatiuza kuti, “Koma anthu oipa ndi onyenga adzaipa chiipire kusokeretsa ndi kusokeretsedwa” (2 Timoteo 3:13). “Koma zindikira ichi kuti masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi cha chibadwidwe, osayanjanitsika, akudierekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu” (2 Timoteo 3:1-4).
“Mtima ndiwo wonyenga koposa ndi wosachiritsika ndani angathe kuudziwa” (Yeremiya 17:9). Yesu anauza ophunzira ake m’mau oti ife tikhoza kuwamvetsa ndi kuwagwiritsa ntchito m’moyo wathu; “Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere” (Mateyu 15:19). “Pakuti monga iye asinka m’kati mwake, ali wotere” (Miyambo 23:7). Yesu ateronso m’Malembo Woyera, “Koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang’ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake” (Mateyu 5:28).
Amayi ndi abambo akufuna moyo wosangalatsa ndipo akuchita zinthu zokwaniritsa zilakolako zao. Iwo aku-sangalala panopa ndipo sadandaula za mawa; sakhudzidwa ndi za chiweruzo cha mlandu wawo pamene adzaima pamaso pa Mulungu. Zosangalatsa zina zomwe atanganidwa nazo ndi chakumwa, mankhwala ozunguza bongo ndi chigololo (dama). Amapita ku zikondwerero ndi zovinavina; amakhala omasuka kudzi-sangalatsa okha. Kumeneko pa kulingalira kwawo amatha kudziletsa pang’ono nthawi zina kulephera kudziletsa kumene. Amakhala ali ndi chakumwa ndi mankhwala ozunguza bongo, zomwe zimawabera kuganiza kwawo kwa umunthu. Satana ndi amene amawaongolera. “Vinyo achita chiphwete, chakumwa chaukali chisokosa; wosochera nazo alibe nzeru” (Miyambo 20:1). “Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga” (Yohane 10:10). Chifukwa cha zotangwanitsa izi makomo amapasuka ndipo ana osalakwa amakhala opanda bambo kapena mayi. Nthawi zina udani wawo umakula mpaka kuphana. “Koma njira ya achiwembu ili makolokoto” (Miyambo 13:15b). Mu Agalatiya 5:19-21 timawerenga kuti “ntchito za thupi ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, madano, kupha, kuledzera, zomwe ndikuchenjezani nazo kuti iwo akuchita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.”
Ndikovomerezeka ndi miyambo ya makolo yosiyana-siyana kuti mnyamata kapena mtsikana akhoza kukhala ndi chibwenzi; amayamba kuchezerana ali ang’ono-ang’ono. Makolo amalimbikitsa zibwenzi zotere poganiza kuti zithandiza mwana wawo, ndipo zibwenzi zawo amachita kuti afanane ndi anzawo m’magulu otchuka. Achinyamata amazolowerana, pasanapite nthawi yaitali. Amayamba kupangana ndi kumapita kuzisangalalo komwe amayambira kusangalatsana ndi dama. Naganiza kuti ena akuchita zotero. “Koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimukokera, ndikumnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima chibala uchimo; ndipo uchimo utakula msinkhu ubala imfa” (Yakobo 1:14-15).
Nthawi zambiri achinyamata saganizira zotsatira za machimo amenewa. Amaganiza kuti adzatha kuthawa chilango cha tchimo. Koma sangathe kugonjetsa mphamvu za Satana. Anyamata amaipitsa atsikana ndipo dongosolo la kubereka ana mwa chiyero limaonongeka. Chikumbumtima chawo chimaipitsidwa ndipo chiyero chawo chimachokanso. Moyo wawo wosachimwa umaonongeka. Chiyambi choyera chomwe chimakometsa chikondi cha mu ukwati chimasokonezeka. Nthawi zambiri amapezeka ali ndi pakati. Zotsatira zake zimachititsa manyazi, kusutsika, kuzungu-zika ndi udindo woyembekezera kudza-samalira mwana. Kawirikawiri oyembe-kezerayo amataya pakatipo. Moyo womwe unapatsidwawo umaonongedwa; ndipo uchimo umaonjezedwa mwa mkaziyo. Nthawi zinanso achinyamata amakhala makolo asanakhwime, zaka za chisangalalo cha chitsikana chawo chimaonongeka; atsikana anzake amayamba kumusala. Makolo ake ndi onse a pabanja lake amakhumudwa, zonsezi ndi chifukwa cha kachisangalalo ka uchimo. Awa ndiwo malipiro a uchimo, “Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa” (Aroma 6:23).
Ukwati ndi wolemekezeka ndiponso dalitso kwa iwo otsatira dongosolo la Mulungu. Mulungu anafuna kuti amuna ndi akazi azikhala okondwa ndi osangalala mu chiyanjano cha ukwati. “Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa” (Ahebri 13:4). Anthu awiri akakondana wina ndi mnzake akhoza kupanga dongosolo la ukwati, koma kukhala limodzi monga mwamuna ndi mkazi mosavomerezeka ndi tchimo pa maso pa Mulungu.
Mulungu analetsa kugonana kwa amuna kapena akazi okha-okha. Kudzera mwa Mose, Mulungu anati, “Usamagonana ndi mwamuna, monga amagonana ndi mkazi; chonyansa ichi” (Levitiko 18:22). Pamene munthu alola chilakolako cha chigololo kukhazikika (kulamulira) maganizo ake, mapeto (matsiriziro) ake amachita zosayenera kuti maganizo ake apherezere (kupha chilakolako chake). Otenthetsana m'thupi amuna okha-okha sachitanso manyazi ndi chikhalidwe chawo chonyansa. Amachitira poyera ndipo amafuna kuti anthu onse avomereze mchitidwe woyipawu. Amanena kuti kugonana kumeneku ndi chikhalidwe chobadwa nacho (kulaza kapena kuyamwira), komabe aliyense adzavomereza mlandu wake. “Pakuti aliyense akachita chilichonse cha zonyansa izi, inde amene azichita adzachotsedwe pakati pa anthu a mtundu wao” (Levitiko 18:29). Za machimo amenewa mu Aroma 1:32 akuti, “Amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zotere ayenera imfa, azichita iwo okha, ndiponso avomerezana ndi iwo akuzichita.”
Matenda ena oopsa kwambiri mwa anthu ndi zotsatira za chikhalidwe chiwerewere. Ntenda yoopsa monga Edzi (magawagawa) ndi matenda ena opatsirana afala (awanda). Kudwala kozunzika ndi imfa yosaneneka zakwera chifukwa cha matendawa. Ophwanya malamulo a Mulungu adza-zunzika chifukwa cha kusamvera kwawo.
“Odala ali oyera mtima; chifukwa adzaona Mulungu” (Mateyu 5:8). Liwu lakuti kudzisunga litanthauza kusachita chigololo kunja kwa ukwati, kusatanganidwa ndi machita-chita onyansa. Kuzisunga ndi lamulo la Mulungu adalipereka kwa anthu kudzera mwa Mose, “Usachite chigololo” (Eksodo 20:14). Yesu akuti “Yense wakusudzula mkazi wake, nakwatira wina, achita chigololo; ndipo iye amene akwatira wosudzulidwayo, achita chigololo” (Luka 16:18).
Tchimo la chigololo limasokoneza munthu pa ntchito zake ndipo limamu-pangitsa kusiya zolinga zomwe zingamu-pindulire ndi kumanyalanyaza udindo wake. Banjanso limanyalanyazidwa ndipo limakhala losasangalala. Kutsutsika ndi machimo otere kumapangitsa munthu kukhala omangika (osakondwa). Pamene mbali inayi mphoto yake yakukhala m`chiyero ndi yopambana. Munthu amene ali muchiyero angathe kukhala ndi mtendere wa mumtima komanso opanda mantha, pamene munthu wosayeretsedwa alibe gawo mu Ufumu wa Mulungu. “Kapena simudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu?” (1 Akorinto 6:9).
Mzimu wa Mulungu udzatsutsa tchimo lake la munthu ndi kumutsogolera ku kulapa. Moyo wonyansa ungasinthike, machimonso angakhululukidwe ngati munthuyo alapa ndi mtima wake wonse. Choyamba ndi kuzindikira tchimo ndi kuopsa kwake pamaso pa Mulungu posayesa kudzilungamitsa iye mwini. Kenako munthu adze kwa Mulungu modzichepetsa, nafotokoza tchimo lake ndi mtima wa chisoni, kupempha chikhululukiro ndi chisomo ndi kubwezera zomwe zinatengedwa ndi kusiya tchimo. Yesu akuti, “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu” (Mateyu 11:28). “Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu” (Yesaya 1:18). “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi” (Masalmo 34:18). Tiyeni titembenuke kuchoka ku njira zathu zoipa ndi kuitana kwa Mulungu nthawi isanathe.