Zimene zalembedwa m'munsi ndi zizindikiro zowonetsa moyo wa kudzikonda. Mzimu Woyera yekha ndi amene angathe kukutanthauzirani izi aliyense payekhapayekha. Pamene mukuwerenga, dziyezeni nokha pa maso penipeni pa Mulungu.
KODI MUMAWONA IZI M'MOYO MWANU:
●Mzimu wobisika wa kunyada kapena wodzikuza powona mwapambana kapena mwapatsidwa udindo; chifukwa chakuti munaphunzira bwino kapenanso mawonekedwe anu; chifukwa cha nzeru kapena mphatso zanu; mzimu umene umadziwona ngati wofunika ndipo wosadalira ena? Miyambo 16:18; 20:6; 25:14; Aroma 12:3; Yakobo 4:6.
●Kukonda kuyamikidwa ndi anthu; kukonda kuti anthu awone zabwino zanu; kukonda kukhala wapamwamba, kudziwonetsera pakulankhula; kudzikuza pamene mwatha kulankhula kapena kupemphera bwino? Yohane 5:44; 12:42,43; 1 Akorinto 13:4.
●Kusonkheza mkwiyo kapena kupsa mtima msanga kumene mumayesa kukulungamitsa ponena kuti ndi mantha kapena kuti munakwiya chifukwa chilungamo sichinachitike; mzimu wokhumudwa msanga; khalidwe lofuna kubwezera mawu oipa pamene mwatsutsidwa? Masalmo 37:8; Mlaliki 7:9; Luka 21:19; Yakobo 1:19.
●Kuchita zokomera iye yekha; wowuma mtima, wa mzimu wosaphunzitsika, wamakangano ndi wolongolola; wankhanza, wonyodola ena; mzimu wokonda kulamulira ena; khalidwe lofunira ena zifukwa pamene wayikidwa pambali; wosachedwa kukwiya; wokonda kusangalatsidwa? Deuteronomo 1:43; Malaki 2:2; Yakobo 3:17; 2 Petro 2:10.
●Mantha akuthupi, mzimu woopa anthu m'malo mwa Mulungu; kuwopa kutonzedwa pokwanitsa udindo wanu, kudzipezera zifukwa pa vuto lako, kuchepesa udindo wako wonse kwa iwo achuma kapena apamwamba; mantha kuti wina adzakhumudwitsa kapena kuchotsa munthu wofunika pamaso pako, mzimu wotengeka? 1 Samueli 15:24; Miyambo 29:25; Agalatiya 2:12; 1 Yohane 4:18.
●Njiru, dumbo lobisika m'mtima mwanu; kusakondwera powona zinthu za ena zikuwa-yendera bwino; khalidwe lokonda kulankhula za zofooka ndi zolakwa za ena m'malo mwa kulankula za mphatso zawo ndi luntha lawo makamaka powona akuyamikiridwa koposa inu? Genesis 26:12-16; 1Samueli 18:8,9; Miyambo 6:34; 14:30; Mateyu 21:15; Aroma 12:9,10.
●Khalidwe losakhulupirika ndi lonyenga; kubisa choonadi; kubisa zolakwa zanu; kudziwonetsera ngati wabwino pamene simuli choncho; kudzi-chepetsa monyenga kapena kuwonjezera nkhani? Masalmo 15:2,3; Yesaya 29:13; Yeremiya 17:9; Mateyu 23:28; Luka 22:48; Machitidwe 5:2,3; 1Timoteo 4:2.
●Kusakhulupirira; mzimu wokhumudwa pa-nthawi yovuta; kusowa mtendere ndi kusadalira mwa Mulungu; kusowa chikhulupiriro ndi kusakhulupirira mwa mulungu, wokhoza kudandaula pamene muli muzowawa, umphawi, kapena chili chonse chimene Mulungu wakulola kuti chikugwereni; kudandaula za m'tsogolo ngati zidzakuyenderani bwino? Yesaya 7:9; Luka 12:28-30; 1 Akorinto 2:14; 2 Akorinto 5:6; Ahebri 11:6; 1 Petro 5:7.
●Zachipamaso, kusowa moyo wa uzimu; kusakhudzika ndi miyoyo yotayika; kusowa mphamvu ya Mulungu? Mateyu 15:14; Timoteo 3:5; Chivumbulutso 2:4; 3:1.
●Kusamala za inu nokha; kukonda kudzi-sangalatsa; kukonda ndalama? Amosi 6:1-6; Luka 12:19-21; 1 Timoteo 6-10,11.
Izi ndi zina za zizindikiro zowonetsa kuti mtima umakonda za thupi. Mwa pemphero, tsegulani mtima wanu kuti kuwunika kwa Mulungu kukuwonetsereni zimene zili m'katimo. “Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nao mayendedwe oipa” (Masalmo 139:23,24).
Mzimu Woyera udzakupangitsani inu povomereza machimo ndi chikhulupiriro kubweretsa moyo wanu wodzikonda ku imfa, povomereza machimo mwa chikhulupiriro. Chotsani zoipa zonse mosayesa kubisa zina. Pokhapo mungathandizidwe.
Kuti ndipulumutsidwe ku kudzikonda kwanga; Ambuye!
Kuti ndidzipereke kwa Inu!
Kuti ndisakhalanse ine konse!,
Koma Khristu wakukhala mwa ine!
“Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika m'kati mwanga” (Masalmo 51:10).