Kodi nchiyani ichi chirikulasa m'moyo mwangamu?
Kufunafuna mtendere ndi mpumulo kosalekezaku?
Kusungulumwa ndimakumvaku?
Ngakhale kuti ndiri mkati mwagulu
Kulira kowawa uku ndi kwakuya ndi kwakukulu;
Kuliraku ndi kwenikweni! Kwenikweni ndithu!
Dziko lachabe kodi ungatonthoze kuliraku?
Kodi chuma chimene wadziunjikiracho chakupezera
iwe mtenderewu?
Ndipo iwenso tatero ndi kulira!
Taona! chuma, kusangalala, ndi kunyada,
Zimene zitchulidwa zangokhala mwadzina chabe!
Izi zilephera kukhutitsa!
Moyo wanga wokondedwawe! Uku kukhalenso kulira
kwako!
Kodi ukuona kuti irnfa ya muyaya ili pafupi,
Ngati Mulungu sakupatsa mtendere?
Iwe ukhale pa mbali ya oikidwa m'manda pamodzi ndi
lye;
Ndipo funitsitsa kumasulidwa ku uchimo,
Ndi kukakhala ndi Iye potsiriza pake!
Taonani ndine waumphawi ndi wotaika m'tchimo!
Wokhala kutali ndi Mulungu m'moyo mwanga!
Mundichitire chifundo, Ambuye!
Tadzatadza liwulo tsopano liyitana dzina langa;
"Wokondedwa wochimwawe, Ndinasenza thonzo lako:
Ndinakhetsa mwazi wanga chifukwa cha iwe!
Kwa iwo akudzawo, ndimawapatsa mpumulo wokoma,
Kufatsa mkati mwa mtima;
Akupeza mwa Ine Ndeka."
Ndirinkudza, Ambuye, ndirinkudza tsopano!
Pansi pa mtanda wanu mwa chimwemwe ndilambira;
Zanga zonse ndidza nazo kwa Inu!
Mtendere wanga wokoma uli pa Kalvari!
Katundu wanga wachoka, moyo wanga wamasuka!
(Apa ndidzakhala kwa muyaya!)
Indedi, Yesu atonthoza kulira kwa mtima wanga;
Indedi moyo wanga uli ndi mudzi kumwamba tsopano,
Ndipo uyembekezera tsiku lalikululo!
Ngati pa nthawi iyi Yesu salikukhala m'mtima mwako, iwe udayeneranso kukhala ndi kulira kwa mtima kobisika kwa moyo wako. Iwe siungathe kukumvetsetsa kuliraku. Ndi moyo wako olirira kwa Mulungu. Iye anaupanga, ndipo mafikira kwa iye "ndipo munthu anakhala ndi moyo" (Genesis 2:7). Ndipo iwo udzakhala kwa muyaya.
Palitu kuthamanga pa dziko lonse lapansi, kuthamanga cha uku ndi uko (Daniele 12:4). Kuzunguzika ndi kufunafuna kupusa kwa zokodweretsa zooneka m’malo moti munthu atembenukire moona kwa Mulungu kupeza yankho lakulira kwa moyo wake. Abambo ndi amayi, anyanmta ndi atsikana ambiri amasiya kukhulupirika ndi ubwino wao ndi chiyembekedzo chosapindulitsa cha kutontholetsa kulira kwa mkati kowawaku. Mukuyetsa kukwaniritsa zokhumbazi ndi chilengedwe cha anthu kutsatira "chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo" (1 Yohane 2:16). Ndi chomvetsa chisoni kuona kuti anthu miyandamiyanda alinkukodwa ndi msampha wa satana wa zilakolako. Pa tsiku lotsiriza iwo adzabaidwa ndi choonadi chakuti satana anali wonyenga, ndi kuti moyo wauchimo ndi wakuthupiwo kunali kudzinamiza chabe. Zoonadi pamapeto pa njira ya moyo wao iwo adzaponyedwa mdzenje la moto wa gahena. Mgahenamo, iwo adzakomana ndi mabvuto osasimbika kwa muyaya (Mateyu 25:41; Chibvumbulutso 20:10-15; 21:8).
Lero lidakali tsiku la chisomo. Nthawi yakuti ochimwa Adze kwa Ambuye kuti akhululukidwe. Lero, ngati moyo wanu uli kulasa ndi kulirira mtendere ndi mpumulo, tembenukirani kwa lye amene moyo wanu umkonda. Tchimo limasiyanitsa ndi Mulungu. Ndipo alipo M'modzi yekha yemwe angakupulumutseni inu, ndipo ameneyo ndi Yesu, Mwana wobadwa yekha wa Mulungu (Yohane 3:16). lye akufunitsitsa atakupulumutsani inu. lye yekha angathe kukupatsani mtendere wa mumtima ndi m'malingaliro anu. lye akukuitanani mofatsa, "ldzani kuno kwa lne nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu" (Mateyu 11:28).
Yesu anazunzika ndi kufa pa mtanda kuombola miyoyo yathu (1 Petro 2:24). lfe tinalitu olakwa. Chilungamo chinafunitsitsa yense wa ife afe, ngakhale imfa ya muyaya. Koma chifukwa cha chiombolo chimenechi, imfa tsopano idamezedwa m'chikhonjetso. Yesu ali "Mwanawankhosa wa Mulungu (wopanda tchimo) amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi" (Yohane 1:29). Iye adaikondetsetsa kwambiri miyoyo ya anthu kuti Iye adafunitsitsa kusiya Atate wake ndi ulemerero wonse ndi kudza pa dziko lapansi. Pano lye anakhala monga munthu nataya moyo wake pa mtanda modzichepetsa kuyeretsa machimo athu, "kuti yense wakukhulupirira akhale nao moyo wosatha mwa lye" (Yohane 3:15).
Anthu ambiri amaganiza kuti adzapulumuka pongokhulupirira mwa Yesu. Zoonadi, tiyenera kukhulupirira mwa Iye, koma “chikhulupiriro chopanda ntchito chili chabe?” (Yakobo 2:20). Yesu mwini anati, “Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba” (Mateyu 7:21).
Ngati moyo wanu suli kupumula, chifukwa cha tchimo m'mtima mwanu, ndi kuti muli kuopa chilango cha muyaya. Idzani kwa Yesu ndi mtima wanu wonse ndipo mumfunse lye kukukhululukirani machimo anu onse ndi kukusambitsani kukuchotserani chosalungania chonse. Tchimo silidzalowa kumwamba. ”Moyo wochimwawo ndiwo udzafa" (Ezekieli 18:4). Koma inu limbanitu mtima, "Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu" (Yesaya 1:18).
Pamene mukuwerenga mau awa, mungamve Mzimu Woyera ali kugogoda mu mtima mwanu. ldza kwa Yesu tsopano! Ali wokonzeka kukukhululukirani ndi kukuombolani inu ku ukapolo wa uchimo ndi mantha.
Kuti muvomere kuitana kwa Mulungu, mutsegule mtima wanu kwa Iye. Ndikuzindikira kuti ndinu wochimwa olephera, ndikuti munatayika kwa muyaya. Khulupirirani kuti chiyembekezo chanu chili mwa Yesu, amene anazunzika ndi kufera machimo anu. Ichi chidzabweretsa chisoni chakuya pa machimo anu. Pamene mulapa ndi kudzipereka kwathunthu kwa Mulungu, Iye adzakukhululukirani. Mudzamva bata ndi mtendere zimene zidzathontholetsa kulira kwa mtima wanu. Ndikofunika kutsatira mwa kumvera pamene Mzimu Woyera ayamba kutsogolera moyo wanu. Iye adzakutsogolerani kumvomereza machimo anu ndi kubwezera zomwe munatenga pamene muyenera kutero. Uku ndi kubadwa mwatsopano kumene Yesu akulankhula mu Yohane 3:3.