Mizinda
Zimene zalembedwa m’munsi ndi zizindikiro zowonetsa moyo wa kudzikonda. Mzimu Woyera yekha ndi amene angathe kukutanthauzirani izi aliyense payekhapayekha. Pamene mukuwerenga, dziyezeni nokha pa maso penipeni pa Mulungu. ●Mzimu wobisika wa kunyada kapena wodzikuza powona mwapambana kapena mwapatsidwa udindo; chifukwa chakuti munaphunzira bwino kapenanso mawonekedwe anu; chifukwa cha nzeru kapena mphatso zanu; mzimu umene umadziwona ngati wofunika ndipo wosadalira ena? Miyambo 16:18; 20:6; 25:14; Aroma 12:3; Yakobo 4:6. ●Kukonda kuyamikidwa ndi anthu; kukonda kuti anthu awone zabwino zanu; kukonda kukhala wapamwamba, kudziwonetsera pakulankhula; kudzikuza pamene mwatha kulankhula kapena kupemphera bwino? Yohane 5:44; 12:42,43; 1 Akorinto 13:4.