Mphamvu

“Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa…” (Aroma 6:23) Tiyeni tinene zoonadi. Zirombo zoopsya kumwa zoledzeretsa, mankhwala ndi chiwerewere ziri nkuopsyeza ndiponso kuononga chimene Mulungu anachilenga kukhala chokoma ndiponso chabwino. Monga mchitidwe wa Octopus wamphamvuyo, izi zimakoka ang’ono komanso aakulu ndi kuwafumbatira. Anthu ambiri amakakamizidwa pambali iliyonse ndi zokhumba zao, monga manyuzi pepala komanso ndi kuitanira kwa television. Maso ndi makutu zimalunjika kumene kuli zosokoneza zokhazokha zomwe zotsatira zake ndi kukhala ndi moyo wa uzimu komanso wa kuthupi wobwerera m’mbuyo. Temberero la chakumwa choledzeretsa, mankhwala ndi chiwerewere zaleka chitsanzo chokoma cha m’midzi yathu popanda kuongoledwa ndipo ziri nkupita ku chionongeko.

Mphamvu 4 minutes

“Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi m’malo a m’katimo” (Masalmo 51:6) Kukhulupirika kumasonyeza kukhala pa choonadi mogwirizana ndi zochita-chita zonse za pa moyo. Kukhulupirika kumachokera mu mtima ndipo ndi chilamulo chokhazikika m’uthenga wa Yesu Kristu. Mulungu amadziwa maganizo ndi zolingirira za mu mtima. Amayang`anira kukhulupirika ngati chilamulo chofunika chifukwa Iye ndi Mulungu wokhulupirika (Deuteronomo 32:4). Iye adzadalitsa kukhulupirika kwathunthu kwa mu mtima wathu. Kodi mumalankhula choonadi pamene mwapezeka kusiyana ndi pamene wina sanadziwe? Kodi mumaonetsa khalidwe lonyenga m’malo mowonetsa moyo wanu weni-weni? Kodi mumagula zinthu pa ngongole pamene mukudziwa kuti simungathe kulipira? Kodi muli okhulupirika molingana ndi chiphunzitso cha Buku Lopatulika?

Mphamvu 4 minutes

Chiyero Chikondi Kukhulupirirana Makomo osangalala Chilakolako Manyazi Mantha Makomo olekana Kusungulumwa Chiyero cha maganizo, chikumbumtima ndi thupi ndi chinthu chopindulitsa m’moyo wa munthu. Ngakhale chiyero chokha sichitanthauza umulungu, koma ndi chipatso cha chikhristu ndi dalitso kwa mtundu wa anthu. Chifukwa cha kuperewera kwa chikhalidwe chabwino amayi ndi abambo lero akulola kukhudzidwa ndi chikhalidwe chimene Buku Lopatulika limanena kuti ndi tchimo. Chikhalidwe chavomerezedwa ngati njira yabwino m’moyo uno ndi anthu ambiri. Chimene Mulungu akunena kuti tchimo, sichikhalanso ngati tchimo. Nanga zotsatira zake zidzakhala zotani?

Mphamvu 6 minutes