Chikondwelero
“Mtendere, uli kuti mtendere - wa maiko athu, m’nyumba zathu, makamaka mtendere wa mitima yathu? Kulira kowawitsa moyo uku kulilira mtendere ktwakhala kuli kumvekabe pakati pa mibadwo yonse; komatu kuliraku nthawi zones kukukulira kulira chifukwa cha kuchuluka zochitika padziko zimene zikupangitsa kuti mtendere usowekedi. M’bale ukuwerengawe, kulira kwa mtima wako ndi kumenekunso kodi? Mkati mwa zosowetsa mtendere ndi zosakhutitsa mtima zonse, kodi umalakalakadi utapeza mtendere wamumtima umene uli opambana zonse? Kodi chuma chimenechi chingapezekedi m’dziko lodzala ndi zopinga, zokhumudwitsa, zosokoneza ndi mabvuto ochuluka? 2. Atipanga ife kukhala ndi mtendere m’dziko lobvutikali. Atitsogolera ife kumalo a phee mchikondi chake chosasintha.