Yesu Bwenzi Lanu Ndili ndi bwenzi. Iye ndi bwenzi loposa onse. Ndi woona ndi wokoma mtima kotero ndikadakonda mutam’dziwa Iye. Dzina lake ndi Yesu. Chinthu chosangalatsa ndi chakuti Iye akufuna kukhala bwenzi lanu. Ntakuuzani za Iye. Nkhaniyi timawerenga m’Buku Lopatulika. Buku Lopatulika ndi loona. Ndi mau a Mulungu. Mulungu ndi amene analenga dziko lapansi ndi zonse zokhala momwemo. Iye ndi Ambuye wakumwamba ndi dziko la pansi. Amapereka moyo ku zinthu zonse. Yesu ndi mwana wa Mulungu. Mulungu anam’tumiza kuchokera kumwamba kubwera padziko lino lapansi kukhala Mpulumutsi wathu wathu. Tsiku lina Iye alinkubweranso. Adzatenga onse okhulupirira Iye kupita nao kwao kumwamba.
March 27, 2019 in Yesu, Chikondi, Chikondi, Kusowa 2 minutes