Nyumbayo

Tikambe kwa Tendoyi pa Intaneti ya Kupatula mwa Msambulezi ndi Mau a Bible

Mizinda

“Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa…” (Aroma 6:23) Tiyeni tinene zoonadi. Zirombo zoopsya kumwa zoledzeretsa, mankhwala ndi chiwerewere ziri nkuopsyeza ndiponso kuononga chimene Mulungu anachilenga kukhala chokoma ndiponso chabwino. Monga mchitidwe wa Octopus wamphamvuyo, izi zimakoka ang’ono komanso aakulu ndi kuwafumbatira. Anthu ambiri amakakamizidwa pambali iliyonse ndi zokhumba zao, monga manyuzi pepala komanso ndi kuitanira kwa television. Maso ndi makutu zimalunjika kumene kuli zosokoneza zokhazokha zomwe zotsatira zake ndi kukhala ndi moyo wa uzimu komanso wa kuthupi wobwerera m’mbuyo. Temberero la chakumwa choledzeretsa, mankhwala ndi chiwerewere zaleka chitsanzo chokoma cha m’midzi yathu popanda kuongoledwa ndipo ziri nkupita ku chionongeko.

Mphamvu 4 minutes
Mawu a pa radio

Bwenzi Lanu

Yesu Bwenzi Lanu Ndili ndi bwenzi. Iye ndi bwenzi loposa onse. Ndi woona ndi wokoma mtima kotero ndikadakonda mutam’dziwa Iye. Dzina lake ndi Yesu. Chinthu chosangalatsa ndi chakuti Iye akufuna kukhala bwenzi lanu. Ntakuuzani za Iye. Nkhaniyi timawerenga m’Buku Lopatulika. Buku Lopatulika ndi loona. Ndi mau a Mulungu. Mulungu ndi amene analenga dziko lapansi ndi zonse zokhala momwemo. Iye ndi Ambuye wakumwamba ndi dziko la pansi. Amapereka moyo ku zinthu zonse. Yesu ndi mwana wa Mulungu. Mulungu anam’tumiza kuchokera kumwamba kubwera padziko lino lapansi kukhala Mpulumutsi wathu wathu. Tsiku lina Iye alinkubweranso. Adzatenga onse okhulupirira Iye kupita nao kwao kumwamba.

Yesu, Chikondi, Chikondi, Kusowa 2 minutes

“Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi m’malo a m’katimo” (Masalmo 51:6) Kukhulupirika kumasonyeza kukhala pa choonadi mogwirizana ndi zochita-chita zonse za pa moyo. Kukhulupirika kumachokera mu mtima ndipo ndi chilamulo chokhazikika m’uthenga wa Yesu Kristu. Mulungu amadziwa maganizo ndi zolingirira za mu mtima. Amayang`anira kukhulupirika ngati chilamulo chofunika chifukwa Iye ndi Mulungu wokhulupirika (Deuteronomo 32:4). Iye adzadalitsa kukhulupirika kwathunthu kwa mu mtima wathu. Kodi mumalankhula choonadi pamene mwapezeka kusiyana ndi pamene wina sanadziwe? Kodi mumaonetsa khalidwe lonyenga m’malo mowonetsa moyo wanu weni-weni? Kodi mumagula zinthu pa ngongole pamene mukudziwa kuti simungathe kulipira? Kodi muli okhulupirika molingana ndi chiphunzitso cha Buku Lopatulika?

Mphamvu 4 minutes

Wokondedwa Moyo’we: Kodi ukudziwa kuti wapezeka wochimwa ndi Mulungu Woyerayo, ndi kuti kwaikidwa kwa iwe kufa? Ngati munthu wochimwa afuna kuithawa imfa ya muyayayi ndi kupulumutsidwa ku nthawi zosatha, iye ayenera kulandira chifundo cha Mulungu’chi. Chifundo chimatiteteza ife pa chirmene tikadalandira. Komatu Mulungu samangoika chifundo chake pa anthu popanda choyenereza ayi, ngakhale kuti chipulumutso nchaulere, chopanda mtengo wake (chosagula) ndiponso chosati nkuchigwirira ntchito. Chotiyenereza chakuti Mulungu atipatse ife chifundo chake chipezeka mu liu limodzi lokha: Lapani.

Kusambira 5 minutes

Kodi nchiyani ichi chirikulasa m’moyo mwangamu? Kufunafuna mtendere ndi mpumulo kosalekezaku? Kusungulumwa ndimakumvaku? Ngakhale kuti ndiri mkati mwagulu Kulira kowawa uku ndi kwakuya ndi kwakukulu; Kuliraku ndi kwenikweni! Kwenikweni ndithu! Dziko lachabe kodi ungatonthoze kuliraku? Kodi chuma chimene wadziunjikiracho chakupezera iwe mtenderewu? Ndipo iwenso tatero ndi kulira! Taona! chuma, kusangalala, ndi kunyada, Zimene zitchulidwa zangokhala mwadzina chabe! Izi zilephera kukhutitsa! Moyo wanga wokondedwawe! Uku kukhalenso kulira kwako! Kodi ukuona kuti irnfa ya muyaya ili pafupi, Ngati Mulungu sakupatsa mtendere? Iwe ukhale pa mbali ya oikidwa m’manda pamodzi ndi lye; Ndipo funitsitsa kumasulidwa ku uchimo, Ndi kukakhala ndi Iye potsiriza pake!

Kusambira 4 minutes
Mawu a pa radio

Masiku Awiri Mu Gehena

Nkhani imodzi ya kutsitsimuka kwa akufa, imene inandichititsa chidwi kwambiri ndi nkhani ya George Lenokisi. Iye anali wakuba wodziwika amene anakhala ku boma la Jefferson County, ankakonda kuba abulu. Iye anali mundende atamangidwa kachiwiri. Poyamba anamangidwa ndi boma la Sedgwick County chifukwa cha mlandu womwewo, kuba abulu. Nthawi yomweyo bokosi lija lidachotsedwa ndipo lidagwiritsidwa ntchito poikamo mtembo wa mkaidi wina. Kenaka adamuchotsa zovala zake za kumanda zija ndipo adamupatsa zovala zake za kundende. Atamuyeza adapeza kuti mwendo wake umodzi udathyoka malo awiri, ndiponso anali ndi mabala. Adakhala kuchipatala miyezi isanu ndi umodzi. Atachira adatumizidwanso kukapitiriza ntchito yake ku ndende.

Tsiku Lina 10 minutes

Zimene zidaoneka monga zinthu zokondweretsa, m’mene akatswiri anayamba kupanga zinthu zaliwiro koposa, katumizidwe ka mau mosabvuta, zochitika zambiri ndi kusintha kwa masiku ano zachititsa dziko ndi anthu kukhala osokonekera. Zinthu zambiri zimene akatswiri anzeru akufufuza-fufuza kuti mwina zingathandize kupanga dziko lapansi kukhala malo abwino kukhalapo zapangitsa moyo kukhala obvuta ndi osokonekera. lnde ngakhale kuti zambiri kwa ife m’moyo uno ndi zosabvuta chifukwa cha izi, zinthu zomwezo zikutipangitsa ife kukhala osowa mtendere ndi osakhazikika m’maganizo ndi m’mitima. Ndife otopetsedwa, ndi odandaula. Ndipo mosabisila. ife tikusowa uphungu ndi chitsogozo, tisowa chitetezo ndi chitsimikizo. Tikusowa, ndipo tikufuna mtendere wamumtima. Ndi Mbuyeyo udidzapita.

Chikondwelero 9 minutes

Nthawi ino muli ndi moyo;mukupuma;mukudya ndi kumwa madzi tsiku ndi tsiku; mukutha kuyendayendakugwira ntchito zanu ndi kumagona. Mwina mukukhala moyo wokandwa mwina wodandaula chifukwa cha mabvuto. Tsiku ndi tsiku dzuŵa likutuluka ndipo likuloŵa; ku malo ena mwana akubadwa, komanso kumalo ena wina akumwalira. PAMENEPA TIONA KUTI ZONSE ZA MOYO WAPANSI PANO NDI ZOSAKHALITSA. KOMA, NDIKADZAFA NDIDZAPITA KUTI? Kaya ndine Mkhristu wofooka kapena wopembedza ku Chisilamu kapena wopembedza ku Chibuda kapena wopembedza ku Chiyuda kapena wopembedza mizimu ya makolo kapena wopembedza chimodzi cha zipembezo zambiri zimene tingazitchule, kapena wosapembedza kumene – NANGA KUMENEKU NDI KUTI? MZIMU WANU SIUDZAFA! MULUMGU AMENE ANALENGA

Moyo Wosokoneka, Mphamvu 3 minutes

Aliyense ayenera kudzifunsa funso lofunikali, “Kodi ndichite chiyani kuti ndipulumutsidwe?” Anthu ambiri ama-khulupirira kuti anapulumutsidwa kale, koma Yesu anati, “Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba: koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba” (Mateyu 7:21). Kuti tipulumuke tiyenera kukhulupirira kuti Yesu adzakhululukira machimo athu. Kenaka tiyenera kulapa machimowo, kukhala ndi moyo wopanda tchimo, ndiponso kukondana wina ndi mzake. Chifukwa cha kuchuluka kwa ziphunzitso zimene zimaphunzitsidwa ndi zipembedzo zosiyana-siyana, funso ili litha kufunsidwa, “Kodi choonadi ndi chiyani?” Kodi “Kubadwa Mwatsopano” Kumatanthauza Chiyani? Ndani Akusowa Kubadwanso Mwatsopano? Kulapa Chikhulupiriro ndi Kumvera

Kusambira 4 minutes

Chiyero Chikondi Kukhulupirirana Makomo osangalala Chilakolako Manyazi Mantha Makomo olekana Kusungulumwa Chiyero cha maganizo, chikumbumtima ndi thupi ndi chinthu chopindulitsa m’moyo wa munthu. Ngakhale chiyero chokha sichitanthauza umulungu, koma ndi chipatso cha chikhristu ndi dalitso kwa mtundu wa anthu. Chifukwa cha kuperewera kwa chikhalidwe chabwino amayi ndi abambo lero akulola kukhudzidwa ndi chikhalidwe chimene Buku Lopatulika limanena kuti ndi tchimo. Chikhalidwe chavomerezedwa ngati njira yabwino m’moyo uno ndi anthu ambiri. Chimene Mulungu akunena kuti tchimo, sichikhalanso ngati tchimo. Nanga zotsatira zake zidzakhala zotani?

Mphamvu 6 minutes

Zimene zalembedwa m’munsi ndi zizindikiro zowonetsa moyo wa kudzikonda. Mzimu Woyera yekha ndi amene angathe kukutanthauzirani izi aliyense payekhapayekha. Pamene mukuwerenga, dziyezeni nokha pa maso penipeni pa Mulungu. KODI MUMAWONA IZI M’MOYO MWANU: ●Mzimu wobisika wa kunyada kapena wodzikuza powona mwapambana kapena mwapatsidwa udindo; chifukwa chakuti munaphunzira bwino kapenanso mawonekedwe anu; chifukwa cha nzeru kapena mphatso zanu; mzimu umene umadziwona ngati wofunika ndipo wosadalira ena? Miyambo 16:18; 20:6; 25:14; Aroma 12:3; Yakobo 4:6. ●Zachipamaso, kusowa moyo wa uzimu; kusakhudzika ndi miyoyo yotayika; kusowa mphamvu ya Mulungu? Mateyu 15:14; Timoteo 3:5; Chivumbulutso 2:4; 3:1. Kuti ndipulumutsidwe ku kudzikonda kwanga; Ambuye!

Kusambira 3 minutes